View Lyrics: Ndinu Mfumu Modal close icon

Viewing lyrics for Ndinu Mfumu by Kaywani.

Chorus
Ndinu Mfumu ya mafumu, Mbuye wathu mwayenera
Kulandila ulemu, mzonse X 2

Verse 1
Munachoka kumwamba, ndikubwera pano padziko,
kuzandifera ine mbuye,
Munasiya ulemelero wanu kumwamba, kuzazunzika chifukwa cha ine,
lero ndiyimba ndili ndi moyo,
ndiimba ndili ndi mphamvu,
kamba ka chikondi chanu,
nchifukwa chake ndiimba

B2C

Verse 2
Mwayenera ulemu, mwayenera matamando,
ndiiyamika dzina lanu mbuye,
Dzina lanu lipambana, dzina lanu ligonjetsa,
palibenso dzina lina,
dzina lanu lakwezedwa, bondo lirilonse ligwade,
kamwa livomereze ku Yesu Khristu ndinu mfumu

B2C

Verse 3
Mbuye wathu wakumwamba ndiyamika dzina lanu
popeza ndikudziwa palibe ofana nanu
inu ndiwamkulu sindingafikire painu
nchifukwa ndili pano kutama ukulu wanu,
mwayenera matamando kunthawi zonse,
ndiyamika dzina lanu ndi mtima wonse, ukulu wanu mbuye unadzala dziko lonse, muziwa zonse, muwona zonse,
chikondi chanu ndichopambana kunthawi zonse,
moti palibe chingatisiyanitse konse, chikondi chanu chimapotsa zonse, ambuye kwainuyo tipereka zonse

B2C

Close